Pamene Nthambi Yoona Zanyengo ya Department of Climate Change and Meteorological Services (DCCMS) yachenjeza aMalawi kuti mvula yamabingu ndinso yamphamvu igwa m’madera ambiri kuyambila Lachinayi mpaka Loweluka sabata ino, nthambiyi yachenjezanso anthu kuti akhale osamala makamaka m’madera omwe madzi amasefukila pafupi pafupi. DCCMS yati mvula yamphamvu ndi yamabinguyi ili ndi kuthekera kobweretsa ziopsezo monga mphezi, […]
The post Khalani osamala pamene mvula ya mphamvu ikugwa – DCCMS appeared first on Malawi 24.